Ndipo ananenanso kwa Iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anai.
Genesis 18:30 - Buku Lopatulika Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Abrahamu adati, “Chonde ndapota nanu, musapse mtima, Ambuye, tsopano ndifunsanso. Nanga mutapezeka anthu olungama 30?” Chauta adati, “Ndikapeza anthu 30, sindidzauwononga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Abrahamu anati, “Pepanitu musandipsere mtima Ambuye, koma mundilole kuti ndiyankhule. Nanga mutapezekamo anthu makumi atatu okha?” Iye anayankha, “Sindidzatero ngati atapezekamo anthu makumi atatu.” |
Ndipo ananenanso kwa Iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anai.
Ndipo anati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye: kapena akapezedwa makumi awiri m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi awiri.
Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao.
Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;
Ndiye Mulungu, ayenera kumuopa kwambiri mu upo wa oyera mtima, ndiye wochititsa mantha koposa onse akumzinga.
Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.
Ndipo Gideoni ananena ndi Mulungu, Mkwiyo wanu usandiyakire, ndinene kamodzi kokha: ndikuyeseni kamodzi kokha ndi chikopa; paume pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame.