kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mzinda wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.
Genesis 18:29 - Buku Lopatulika Ndipo ananenanso kwa Iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ananenanso kwa Iye nati, Kapena akapezedwa makumi anai m'menemo. Ndipo anati, Sindidzachita chifukwa cha makumi anai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adafunsanso kuti, “Nanga pakapezeka anthu olungama 40 okha?” Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 40, sindidzauwononga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenakanso anayankhula kwa Iye nati, “Bwanji atangopezekamo anthu 40 okha?” Iye anayankha, “Chifukwa cha anthu 40 amenewa, sindidzatero.” |
kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mzinda wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.
Ndipo anati, Asakwiyetu Ambuye, ndipo ndidzanenanso: kapena akapezedwa makumi atatu m'menemo? Ndipo anati, Ndikapeza makumi atatu m'menemo sindidzachita.
mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.