kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mzinda wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.
Genesis 18:27 - Buku Lopatulika Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayankha Abrahamu nati, Taonanitu, ndadziyesera kunena kwa Ambuye, ine ndine fumbi ndi phulusa: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abrahamu adalankhulanso, adati, “Chonde, ndalimba mtima pakulankhula nanu chotere, Ambuye. Inetu ndine munthu chabe pamaso panu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Abrahamu anayankhulanso nati, “Tsono poti ndalimba mtima kuyankhula ndi Ambuye, ngakhale kuti ndine fumbi ndi phulusa chabe, |
kapena akaperewera asanu pa olungama makumi asanuwo; kodi mudzaononga mzinda wonse chifukwa cha kuperewera asanu? Ndipo anati, Ndikapeza makumi anai ndi asanu sindidzauononga.
Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.
m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.
ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kuchita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zachuluka pamutu pathu, ndi kupalamula kwathu kwakula kufikira mu Mwamba.
kopambana kotani nanga iwo akukhala m'nyumba zadothi, amene kuzika kwao kuli m'fumbi, angothudzulidwa ngati njenjete.
Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba?
fumbi ndi kubwera pansi pomwe linali kale, mzimu ndi kubwera kwa Mulungu amene anaupereka.
Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.
Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu.
Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.