Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 18:26 - Buku Lopatulika

Ndipo anati Yehova, Ndikapeza mu Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mzinda, ndidzasiya malo onse chifukwa cha iwo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anati Yehova, Ndikapeza m'Sodomu olungama makumi asanu m'kati mwa mudzi, ndidzasiya malo onse chifukwa cha iwo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta adayankha kuti, “Ndikapeza anthu 50 osachimwa m'Sodomu, ndidzauleka mzinda wonsewo osauwononga, chifukwa cha anthu 50 amenewo.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yehova anati, “Nditapeza anthu makumi asanu olungama mu mzinda wa Sodomu, ndidzasiya malo onsewo osawawononga chifukwa cha iwo.”

Onani mutuwo



Genesis 18:26
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova adati, Kodi ndidzabisira Abrahamu chimene ndichita?


Popeza ngakhale anthu anu Israele akunga mchenga wa kunyanja, otsala ao okhaokha adzabwera; chionongeko chatsimikizidwa chilungamo chake chisefukira.


Tsiku limenelo Israele ndi Ejipito ndi Asiriya atatuwa, adzakhala mdalitso pakati padziko lapansi;


Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake.


Atero Yehova, Monga vinyo watsopano apezedwa m'tsango, ndipo wina ati, Usaliononge, pakuti muli mdalitso m'menemo, ndidzachita chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawaononge onse.


Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.


Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe.


Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.