Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza.
Genesis 18:22 - Buku Lopatulika Ndipo anthuwo anatembenuka nachoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthuwo anatembenuka nachoka kumeneko, napita kunka ku Sodomu. Koma Abrahamu anaimabe pamaso pa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu aja adachoka, napita ku Sodomu, koma Abrahamu adatsarira ndi Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu aja anatembenuka nʼkumapita, kulowera ku Sodomu, koma Abrahamu anali chiyimirire pamaso pa Yehova. |
Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza.
Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.
Potero Iye adati awaononge, pakadapanda Mose wosankhika wake, kuima pamaso pake pogamukapo, kubweza ukali wake ungawaononge.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.
Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.
Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe.
Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira padzanja lamanja la Mulungu,
Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse;