Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa cha iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe.
Genesis 18:15 - Buku Lopatulika Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; chifukwa anaopa. Ndipo anati, Iai; koma unaseka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Sara anakana, nati, Sindinasekai; chifukwa anaopa. Ndipo anati, Iai; koma unaseka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Sara adakana chifukwa cha mantha, adati, “Sindidaseke.” Koma Iye adati, “Inde, unaseka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Sara ndi mantha ananama nati, “Sindinaseke.” Koma Iye anati, “Inde iwe unaseka.” |
Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa cha iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe.
Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.
Ndipo anthuwo anauka kuchokera kumeneko nayang'ana ku Sodomu; ndipo Abrahamu ananka nao kuwaperekeza.
Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako? Ndipo anati, Sindidziwai: kodi ndine woyang'anira mphwanga?
Koma ananena naye, Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! Tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa? Pa ichi chonse Yobu sanachimwe ndi milomo yake.
Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwake kuti alikuganizira chomwecho mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu?
Pamenepo mdzakazi wapakhomoyo ananena kwa Petro, Kodi suli iwenso wa ophunzira a munthu uyu? Iyeyu ananena, Sindine.
ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.
Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;
musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,