ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba?
Genesis 18:13 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, Bwanji anaseka Sara, kuti, Kodi ndidzabala ine ndithu, ine amene ndakalamba? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta adafunsa Abrahamu kuti, “Chifukwa chiyani Sara amaseka ndi kunena kuti, ‘Ine monga ndakalambiramu kungatheke bwanji kukhala ndi mwana?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, “Nʼchifukwa chiyani Sara anaseka nʼkumati, ‘Moti ine nʼkudzakhaladi ndi mwana mmene ndakalambiramu?’ |
ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba?
Kodi chilipo chinthu chomkanika Yehova? Pa nthawi yoikidwa ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.
Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? Pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna mu ukalamba wake.
ndipo sanasowe wina achite umboni za munthu; pakuti anadziwa Iye yekha chimene chinali mwa munthu.