Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani.
Genesis 17:27 - Buku Lopatulika Ndipo amuna onse a m'nyumba mwake obadwa m'nyumba, ndi ogulidwa ndi ndalama kwa alendo, anadulidwa pamodzi naye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo amuna onse a m'nyumba mwake obadwa m'nyumba, ndi ogulidwa ndi ndalama kwa alendo, anadulidwa pamodzi naye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pamodzi ndi anthu aamuna onse, amuna obadwira m'banja mwake ndiponso ena amene adaŵagula ndi ndalama kwa alendo, onsewo adaumbalidwa pamodzi ndi iyeyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense wamwamuna wa pa banja pa Abrahamu, kuphatikizapo iwo amene anabadwira pa banja pomwepo kapena akapolo ogula ndi ndalama kwa alendo, anachita mdulidwe. |
Pamene anamva Abramu kuti mphwake anagwidwa, anatuluka natsogolera anyamata ake opangika, obadwa kunyumba kwake, mazana atatu kudza khumi ndi asanu ndi atatu, nawalondola kufikira ku Dani.
Ili ndi pangano langa limene uzisunga pakati pa Ine ndi iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako: azidulidwa amuna onse a mwa inu.
Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.