Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.
Genesis 17:26 - Buku Lopatulika Tsiku lomwelo anadulidwa Abrahamu ndi Ismaele mwana wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsiku lomwelo anadulidwa Abrahamu ndi Ismaele mwana wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku limeneli Abrahamu ndi mwana wake Ismaele adaumbalidwa, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Onse, Abrahamu ndi mwana wake Ismaeli, anachita mdulidwe tsiku limodzi. |
Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.
Ndipo Ismaele mwana wake anali wa zaka khumi ndi zitatu pamene anadulidwa m'khungu lake.
Ndipo amuna onse a m'nyumba mwake obadwa m'nyumba, ndi ogulidwa ndi ndalama kwa alendo, anadulidwa pamodzi naye.