Genesis 17:22 - Buku Lopatulika Ndipo analeka kunena naye, ndipo Mulungu anakwera kuchokera kwa Abrahamu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analeka kunena naye, ndipo Mulungu anakwera kuchokera kwa Abrahamu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mulungu atatha kulankhula ndi Abrahamu, adamsiya pomwepo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atatha kuyankhula, Mulungu anamuchokera Abrahamu. |
Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israele, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kuchokera kumwamba.
Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera.
Pakuti kunali, pakukwera lawi la moto paguwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m'lawi la paguwalo; ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi.
Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lake, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo unatuluka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda chotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pake.