ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;
Genesis 17:20 - Buku Lopatulika Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma kunena za Ismaeleyu, ndidzamdalitsa, ndipo ndidzampatsa ana ambiri pamodzi ndi zidzukulu. Adzakhala bambo wa mafumu khumi ndi aŵiri, ndipo zidzukulu zake ndidzakhala mtundu waukulu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma za Ismaeli, ndamva. Ndidzamudalitsadi, ndipo adzakhala ndi zidzukulu zambiri. Iye adzakhala kholo la mafumu khumi ndi awiri ndipo mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu wa anthu. |
ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;
Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; chifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Mulungu Wamphamvuyonse akudalitse iwe, akubalitse iwe, akuchulukitse iwe, kuti ukhale khamu la anthu: