Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika.
Genesis 17:15 - Buku Lopatulika Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamutcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usam'tcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mkazi wakoyu usamutchulenso kuti Sarai. Tsopano dzina lake ndi Sara. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mulungu anatinso kwa Abrahamu, “Sarai mkazi wako, sudzamutchanso Sarai; dzina lake lidzakhala Sara. |
Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika.
Ndipo mwamuna wosadulidwa, wosadulidwa khungu lake, munthuyo amsadze mwa anthu a mtundu wake; waphwanya pangano langa.
Ndipo ndidzamdalitsa iye, ndiponso ndidzakupatsa iwe mwana wamwamuna wobadwa mwa iye, inde, ndidzamdalitsa iye, ndipo adzakhala amake amitundu, mafumu a anthu adzatuluka mwa iye.
Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.
Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova.
Mverani Ine, inu amene mutsata chilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang'anani kuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo.