Ndipo anati Mulungu, Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo;
Genesis 17:11 - Buku Lopatulika Muzidula khungu lanu; ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa Ine ndi inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muzidula khungu lanu; ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa Ine ndi inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kuyambira tsopano muziwumbalidwa. Chimenechi chidzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuyambira tsopano muzichita mdulidwe ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi iwe. |
Ndipo anati Mulungu, Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo;
Ndipo Davide anatumiza mithenga kwa Isiboseti mwana wa Saulo, nati, Undipatse mkazi wanga Mikala amene ndinadzitomera ndi nsonga za makungu za Afilisti zana limodzi.
Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paska, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko.
Koma Zipora anatenga mpeni wamwala, nadula khungu la mwana wake, naliponya pa mapazi ake; nati, Pakuti iwe ndiwe mkwati wanga wamwazi. Ndipo Iye anamleka.
Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo aakulu aja khumi ndi awiri.
iye ndipo analandira chizindikiro cha mdulidwe, ndicho chosindikiza chilungamo cha chikhulupiriro, chomwe iye anali nacho asanadulidwe; kuti kotero iye akhale kholo la onse akukhulupirira, angakhale iwo sanadulidwe, kuti chilungamo chiwerengedwe kwa iwonso;