Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.
Genesis 16:16 - Buku Lopatulika Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismaele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi, pamene Hagara anambalira Abramu Ismaele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abramu anali wa zake 86 pa nthaŵi imeneyo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Hagara anamubalira Ismaeli nʼkuti Abramuyo ali ndi zaka 86. |
Ndipo anamuka Abramu monga Yehova ananena kwa iye, ndipo Loti anamuka pamodzi naye: ndipo Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi awiri kudza zisanu, pamene anatuluka mu Harani.
Ndipo Hagara anambalira Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anatcha dzina la mwana wake amene anambalira iye Hagara, Ismaele.
Ndipo Sarai mkazi wake wa Abramu anatenga Hagara mdzakazi wake wa ku Ejipito, Abramu atakhala m'dziko la Kanani zaka khumi, nampereka iye kwa Abramu mwamuna wake, kuti akhale mkazi wake.
Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.
Ndipo Ismaele mwana wake anali wa zaka khumi ndi zitatu pamene anadulidwa m'khungu lake.
Zaka za moyo wa Ismaele ndi izi: zaka zana limodzi kudza makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri: ndipo iye anamwalira, natengedwa akhale ndi a mtundu wake.