Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m'chipululu, nakhala wauta.
Genesis 16:12 - Buku Lopatulika Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lake lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ake onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lake lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ake onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mwana wako adzakhala ndi mtima wa chilombo, adzadana ndi aliyense, ndipo anthu onse adzadana naye. Adzakhala akudana ndi abale ake onse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye adzakhala munthu wa khalidwe ngati mʼmbulu wamisala; adzadana ndi aliyense ndipo anthu onse adzadana naye, adzakhala mwaudani pakati pa abale ake onse.” |
Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m'chipululu, nakhala wauta.
Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwake kwa Ejipito, pakunka ku Asiriya: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse.
Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako.
Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito.
Taonani, ngati mbidzi za m'chipululu atulukira kuntchito zao, nalawirira nkufuna chakudya; chipululu chiwaonetsera chakudya cha ana ao.