Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.
Genesis 16:11 - Buku Lopatulika Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Taona, uli ndi pakati, ndipo udzabala mwana wamwamuna; nudzamutcha dzina lake Ismaele; chifukwa Yehova anamva kusauka kwako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Popitiriza mau mngeloyo adati, “Tsopano uli pafupi kukhala ndi mwana wamwamuna, udzamutche Ismaele, ndiye kuti Chauta wamva kulira kwako pa zovuta zako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mngelo wa Yehova uja anamuwuzanso kuti, “Ndiwe woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna. Udzamutcha dzina lake Ismaeli, pakuti Yehova wamva kulira chifukwa cha kuzunzika kwako. |
Ndipo Mulungu anati, Koma Sara mkazi wako adzakubalira iwe mwana wamwamuna; ndipo udzamutcha dzina lake Isaki; ndipo ndidzalimbikitsa naye pangano langa, kuti likhale pangano la nthawi zonse, la ku mbeu zake za pambuyo pake.
Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? Usaope; chifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.
Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito.
Amkonzeratu khwangwala chakudya chake ndani, pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu, naulukauluka osowa chakudya?
Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.
Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;
Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako.
Chifukwa chake Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu chizindikiro; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamutcha dzina lake Imanuele.
Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
Ndipo taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.
Ndipo iye anafunsa cholemberapo, nalemba, kuti, Dzina lake ndi Yohane. Ndipo anazizwa onse.
Ndipo panali pamene nthawi yake inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Samuele, nati, Chifukwa ndinampempha kwa Yehova,