Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.
Genesis 16:10 - Buku Lopatulika Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzachulukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Ndidzachulukitsa ndithu mbeu zako, kuti unyinji wao sudzawerengeka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka, zosaŵerengeka.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri zoti munthu sangaziwerenge.” |
Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.
Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa iye, Bwera kwa wakuka wako, udzichepetse wekha pamanja pake.
Koma za Ismaele, ndamvera iwe: taona, ndamdalitsa iye, ndipo ndidzamchulukitsa iye ndithu; adzabala akalonga khumi ndi awiri, ndipo ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patali, monga pakugwa muvi: chifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ake nalira.
Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; chifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukulu.
M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pake anawapulumutsa; m'kukonda kwake ndi m'chisoni chake Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Kulibe munthu anaona Mulungu nthawi zonse; Mwana wobadwa yekha wakukhala pa chifuwa cha Atate, Iyeyu anafotokozera.
amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.
Pamenepo anadza mthenga wa Yehova, nakhala patsinde pa thundu wokhala mu Ofura, wa Yowasi Mwabiyezere; ndi mwana wake Gideoni analikuomba tirigu m'mopondera mphesa, awabisire Amidiyani.
Ndipo Yehova ananena naye, Popeza Ine ndidzakhala nawe udzakantha Amidiyani ngati munthu mmodzi.