Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzake: koma mbalame sanazidule.
Genesis 15:17 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene litalowa dzuwa ndi kudza mdima, taonani, ng'anjo yofuka utsi ndi muuni wamoto unadutsa pakati pa mabanduwo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene litalowa dzuwa ndi kudza mdima, taonani, ng'anjo yofuka utsi ndi muuni wamoto wapita pakati pa mabanduwo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dzuŵa litangoloŵa, kachisisira katagwa, mwadzidzidzi padaoneka mphika wogaduka ndi moto, pamodzi ndi nsakali yoyaka, ndipo ziŵirizi zidadutsa pakati pa nyama zodulidwa zija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzuwa litalowa ndipo mdima utagwa, panaoneka mʼphika wofuka nthunzi ya moto ndi sakali yoyaka ndipo zinadutsa pakati pa zidutswa za nyama zija. |
Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzake: koma mbalame sanazidule.
M'mphuno mwake munatuluka utsi, ndi moto wotuluka m'kamwa mwake unaononga; makala anayaka nao.
Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nutentha nsembe yopsereza, ndi nkhuni, ndi miyala, ndi fumbi, numwereretsa madzi anali mumchera.
Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m'mwamba ndi moto paguwa la nsembe yopsereza.
Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.
Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.
Chifukwa cha Ziyoni sindidzakhala chete, ndi chifukwa cha Yerusalemu sindidzapuma, kufikira chilungamo chake chidzatuluka monga kuyera, ndi chipulumutso chake monga nyali yoyaka.
limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, m'ng'anjo ya chitsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwachita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu;
Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m'ng'anjo yamoto, mu Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.
Pakuti kunali, pakukwera lawi la moto paguwa la nsembe kumwamba, mthenga wa Yehova anakwera m'lawi la paguwalo; ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere; nagwa iwowa nkhope zao pansi.
Pamenepo mthenga wa Yehova anatambasula nsonga ya ndodo inali m'dzanja lake, nakhudza nyamayi ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo unatuluka moto m'thanthwe nunyeketsa nyama ndi mikate yopanda chotupitsa; ndi mthenga wa Yehova anakanganuka pamaso pake.