Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzake: koma mbalame sanazidule.
Genesis 15:11 - Buku Lopatulika Pamene miimba inatsikira panyama, Abramu anaingitsa iyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene miimba inatsikira panyama, Abramu anaingitsa iyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Miphamba idadzatera kuti idye nyama zimene adaaphazo, koma Abramu adaipirikitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene miphamba inabwera kuti itole nyama ija, Abramu anayipirikitsa. |
Ndipo anatenga iye zonse zimenezo, nazidula pakati, naika bandu popenyana ndi linzake: koma mbalame sanazidule.
Ndipo linalinkulowa dzuwa, ndi tulo tatikulu tinamgwera Abramu: ndipo taonani, kuopsa kwa mdima waukulu kunamgwera iye.
nuziti, Atero Ambuye Yehova, Chiombankhanga chachikulu ndi mapiko aakulu, ndi maphiphi aatali, odzala nthenga cha mathothomathotho, chinafika ku Lebanoni, nkutenga nsonga ya mkungudza,
Panalinso chiombankhanga china chachikulu, ndi mapiko aakulu, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unachipindira mizu yake, nuchilunjikitsira zake, kuchokera pookedwa pake, kuti chiuthirire madzi.
Ndipo m'kufesa kwake zina zinagwa m'mbali mwa njira, ndipo zinadza mbalame, nkulusira izo.