Zaka khumi ndi ziwiri iwo anamtumikira Kedorilaomere, chaka chakhumi ndi chitatu anapanduka.
Genesis 14:5 - Buku Lopatulika Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu mu Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu mu Hamu, ndi Aemimu mu Savekiriyataimu, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu m'Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu m'Hamu, ndi Aemimu m'Savekiriyataimu, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa chaka chakhumi ndi chinai Kedorilaomere pamodzi ndi anzake ogwirizana nawo, adadza ndi nkhondo nagonjetsa Arefaimu amene ankakhala ku Asiteroti-karanaimu, Azuzimu amene ankakhala ku Hamu, ndi Aemimu amene ankakhala ku chigwa cha Kiriyataimu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mʼchaka cha khumi ndi chinayi, Kedorilaomere mogwirizana ndi mafumu ena aja anapita kukagonjetsa Arefaiwa ku Asiteroti-karanaimu, Zuzimu wa ku Hamu, Aemi wa ku Savekiriataimu |
Zaka khumi ndi ziwiri iwo anamtumikira Kedorilaomere, chaka chakhumi ndi chitatu anapanduka.
Ndipo atatu a mwa makamu atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti linamanga zithando m'chigwa cha Refaimu.
Ndipo atatu a akulu makumi atatu anatsikira kuthanthwe kwa Davide, ku phanga la Adulamu; ndi nkhondo ya Afilisti idamanga misasa m'chigwa cha Refaimu.
Ndipo anapeza podyetsa ponenepetsa ndi pabwino, ndipo dzikoli ndi lachitando ndi lodikha ndi losungikamo, pakuti okhalako kale ndiwo a Hamu.
Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosacheka, ndi dzanja lake lilikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'chigwa cha Refaimu.
Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.
atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, wakukhala mu Asitaroti, ku Ederei.
(Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).
Ndi chotsalira cha Giliyadi, ndi Basani lonse, dziko la Ogi, ndinapatsa hafu la fuko la Manase; dziko lonse la Arigobu, pamodzi ndi Basani. (Ndilo lotchedwa dziko la Arefaimu.
kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lija la Yordani; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku cholowa chake, chimene ndinakupatsani.
Nalandanso malire a Ogi mfumu ya Basani wotsala wa Arefaimu, wokhala ku Asitaroti ndi ku Ederei,
ufumu wonse wa Ogi mu Basani, wa kuchita ufumu mu Asitaroti, ndi mu Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.
ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi mu Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.
ndi zonse anachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basani wokhala ku Asitaroti.