Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Genesis 14:23 - Buku Lopatulika

kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale chingwe cha nsapato, ngakhale kanthu kalikonse kako, kuti unganene, Ndamlemeretsa Abramu;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

kuti sindidzatenga ngakhale thonje ngakhale chingwe cha nsapato, ngakhale kanthu kalikonse kako, kuti unganene, Ndamlemeza Abramu;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

kuti sindidzatenga zinthu zako mpang'ono pomwe. Sindidzatenga ngakhale mbota kapena chingwe chomangira nsapato, kuti ungamadzanene kuti, ‘Abramu ndidamulemeza ndine.’

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

kuti sindidzalandira kanthu kalikonse kako, ngakhale utakhala ulusi chabe kapena chingwe cha nsapato, kuopa kuti ungamanene kuti, ‘Ndamulemeretsa Abramu.’

Onani mutuwo



Genesis 14:23
8 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowe kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.


Koma anati, Pali Yehova, amene ndiima pamaso pake, sindidzalandira kanthu. Ndipo anamkakamiza achilandire, koma anakana.


Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Naamani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ake chimene anabwera nacho; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye.


ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira chingwe cha nsapato yake.


Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana.


Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.