Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
Genesis 14:21 - Buku Lopatulika Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge chuma iwe wekha. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mfumu ya Sodomu ndipo inati kwa Abramu, Ndipatse ine anthu, nutenge chuma iwe wekha. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komanso mfumu ya ku Sodomu idapempha Abramu kuti “Zinthu zonse mudatengazi, musunge, koma anthu anga okhaŵa mundipatse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu ya Sodomu inati kwa Abramu, “Ine undipatse anthu okhawo, koma katundu akhale wako.” |
Ndipo Abramu anatenga Sarai mkazi wake, ndi Loti mwana wa mphwake, ndi chuma chao chimene anasonkhanitsa, ndi miyoyo imene anabala mu Harani; natuluka kunka ku dziko la Kanani, ndipo anadza ku dziko la Kanani.
Chigwa cha Sidimu chinali ndi zitengetenge thoo; ndipo anathawa mafumu a ku Sodomu ndi Gomora nagwa m'menemo: amene anatsala anathawira kuphiri.
ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.
Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi
Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za chakudya chanu, ndi cha ana anu ndi mabanja anu.