Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.
Genesis 13:17 - Buku Lopatulika Tauka, nuyendeyende m'dzikoli m'litali mwake ndi m'mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tauka, nuyendeyende m'dzikoli m'litali mwake ndi m'mimba mwake; chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe limenelo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nyamuka tsopano, uyendere dziko lonselo, chifukwa ndakupatsa,” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzuka ndipo uyendere dziko lonseli mulitali ndi mulifupi pakuti ndalipereka kwa iwe.” |
Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.
chifukwa kuti dziko lonse limene ulinkuona, ndidzakupatsa iwe ndi mbeu yako nthawi yonse.
Ndipo anati kwa iye, Ine ndine Yehova amene ndinatulutsa iwe mu Uri wa kwa Akaldeya, kuti ndikupatse iwe dziko limeneli likhale lakolako.
Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.
Taonani, Yehova anaima pamwamba pake, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isaki; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako;
Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.
Koma Yehova analeza nao mtima, nawachitira chifundo, nawatembenukira; chifukwa cha chipangano chake ndi Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pake.