Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
Genesis 13:14 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang'anire kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, ndi kumadzulo: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova anati kwa Abramu, atalekana naye Loti, Tukulatu maso ako, nuyang'anire kuyambira kumene uliko, kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, ndi kumadzulo: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Loti atachoka, Chauta adauza Abramu kuti, “Uyang'ane bwino kumpoto, kumwera, kuvuma ndi kuzambwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Loti atachoka, Yehova anati kwa Abramu, “Kuchokera pamene ulipo tayangʼanayangʼana cha kumpoto, kummwera, kummawa ndi kumadzulo. |
Ndipo Loti anatukula maso ake nayang'ana chigwa chonse cha Yordani kuti chonsecho chinali ndi madzi ambiri, asanaononge Yehova Sodomu ndi Gomora, monga munda wa Yehova, monga dziko la Ejipito pakunka ku Zowari.
mbeu zako zidzakhala monga fumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.
Tukula maso ako kuunguzaunguza, nuone; onsewa asonkhana pamodzi, nadza kwa iwe. Pali Ine, ati Yehova, iwe ndithu udzadziveka wekha ndi iwo onse, monga ndi chokometsera, ndi kudzimangira nao m'chuuno ngati mkwatibwi.
Tukula maso ako uunguzeunguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako aamuna adzachokera kutali, ndi ana ako aakazi adzaleredwa pambali.
Kwera kumwamba ku Pisiga, nukweze maso ako kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera, ndi kum'mawa, nuyang'ane ndi maso ako; popeza sudzaoloka Yordani uyo.
Ndipo Mose anakwera kuchokera ku zidikha za Mowabu, kunka kuphiri la Nebo, pamwamba pa Pisiga, popenyana ndi Yeriko. Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse la Giliyadi, kufikira ku Dani;