Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke.
Genesis 12:20 - Buku Lopatulika Ndipo Farao analamulira anthu ake za iye; ndipo anamperekeza iye m'njira ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao analamulira anthu ake za iye; ndipo anamperekeza iye m'njira ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao adalamula anthu ake, ndipo iwowo adatulutsa Abramu ndi mkazi wake m'dzikomo, pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Farao analamula asilikali ake ndipo iwo anamutulutsa Abramu pamodzi ndi mkazi wake ndi zonse anali nazo. |
Chifukwa chanji unati, Ndiye mlongo wanga? Kotero ndinamtenga iye akhale mkazi wanga; tsopano suyu mkazi wako; mtenge nuchoke.
Ndipo anakwera Abramu kuchoka ku Ejipito, iye ndi mkazi wake, ndi zonse anali nazo, ndi Loti pamodzi naye, kunka ku dziko la kumwera.