Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa cha iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe.
Genesis 12:14 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene Abramu analowa mu Ejipito, Aejipito anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene Abramu analowa m'Ejipito, Aejipito anaona kuti mkazi anali wokongola kwambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abramu ataoloka malire kuloŵa mu Ejipito, Aejipito adaonadi kuti mkazi wake ndi wokongola kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Abramu anafika ku Igupto, Aigupto aja anaona kuti Sarai anali mkazi wokongoladi. |
Uzikanenatu, kuti iwe ndiwe mlongo wanga: kuti chidzakhala chabwino ndi ine, chifukwa cha iwe, ndi kuti moyo wanga usungike ndi iwe.
Ndipo akalonga ake a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwake kwa Farao.
Ndipo pamene anaona mkaziyo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m'maso, mtengo wolakalakika wopatsa nzeru, anatenga zipatso zake, nadya, napatsanso mwamuna wake amene anali naye, nadya iyenso.
Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.
kuti ana aamuna a Mulungu anayang'ana ana aakazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasankha.
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.