Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamutcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara.
Genesis 11:29 - Buku Lopatulika Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abramu ndi Nahori adakwatira. Abramu adakwatira Sarai, ndipo Nahori adakwatira Milika mwana wa Harani, amene analinso bambo wake wa Isika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abramu ndi Nahori onse anakwatira. Dzina la mkazi wa Abramu linali Sarai, ndipo la mkazi wa Nahori linali Milika. Iyeyu ndi Isika abambo awo anali Harani. |
Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamutcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara.
Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga.
Ndipo panali zitapita izi, anauza Abrahamu kuti, Taonani, Milika iyenso anambalira Nahori mphwako ana;
Ndimo Betuele anabala Rebeka: amenewa asanu ndi atatu Milika anambalira Nahori mphwake wa Abrahamu.
Ndipo mnyamatayo anatenga ngamira khumi za mbuyake, namuka: chifukwa kuti chuma chonse cha mbuyake chinali m'dzanja lake: ndipo anachoka namuka ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
Ndipo panali, asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anambala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake.
Ndipo mkaziyo anati kwa iye, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wamwamuna wa Milika, amene anambalira Nahori.