ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri, atabala Nahori, nabala ana aamuna ndi aakazi.
Genesis 11:24 - Buku Lopatulika Ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka makumi awiri kudza zisanu ndi zinai, nabala Tera: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka makumi awiri kudza zisanu ndi zinai, nabala Tera: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nahori ali wa zaka 29, adabereka mwana dzina lake Tera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene Nahori anali ndi zaka 29, anabereka Tera. |
ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri, atabala Nahori, nabala ana aamuna ndi aakazi.
ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza khumi ndi zisanu ndi zinai, atabala Tera, nabala ana aamuna ndi aakazi.
Kuwerenga kwake ndiko: mbale zagolide makumi atatu, mbale zasiliva chikwi chimodzi, mipeni makumi awiri mphambu isanu ndi inai;
Ndipo Yoswa ananena ndi anthu onse, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kale lija makolo anu anakhala tsidya lija la mtsinje, ndiye Tera, atate wa Abrahamu ndi atate wa Nahori; natumikira milungu ina iwowa.