ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakisadi, nabala ana aamuna ndi aakazi.
Genesis 11:10 - Buku Lopatulika Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakisadi, chitapita chigumula zaka ziwiri; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakisadi, chitapita chigumula zaka ziwiri; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nayi mibadwo yofumira mwa Semu: Patangopita zaka ziŵiri chitatha chigumula, Semu ali wa zaka 100, adabereka mwana dzina lake Aripakisadi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nayi mibado yochokera kwa Semu. Patapita zaka ziwiri chitatha chigumula, Semu ali ndi zaka 100, anabereka Aripakisadi. |
ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakisadi, nabala ana aamuna ndi aakazi.
Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti.