Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.
Genesis 10:32 - Buku Lopatulika Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu padziko lapansi, chitapita chigumula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu pa dziko lapansi, chitapita chigumula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Onseŵa ndiwo mafuko a zidzukulu za Nowa potsata mibadwo yao ndi mitundu yao. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idatuluka mwa mafuko a Nowa ameneŵa, chitatha chigumula chija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija. |
Mibadwo ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti, ndi iyi; kwa iwo ndipo kunabadwa ana aamuna, chitapita chigumula chija.
Amenewa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana aamuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani.
Amenewa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.
ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;