Genesis 10:29 - Buku Lopatulika ndi Ofiri ndi Havila, ndi Yobabu; onse amenewa ndi ana a Yokotani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi Ofiri ndi Havila, ndi Yobabu; onse amenewa ndi ana a Yokotani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onseŵa anali ana a Yokotani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani. |
Dzina la woyamba ndi Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide;
Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwake kwa Ejipito, pakunka ku Asiriya: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse.
Yehosafati anamanga zombo za ku Tarisisi kukatenga golide ku Ofiri; koma sizinamuke, popeza zinaphwanyika pa Eziyoni-Gebere.
Ndipo iwo anafika ku Ofiri, natengako golide matalente mazana anai mphambu makumi awiri, nafika naye kwa mfumu Solomoni.
ndi abale ao, akulu a nyumba za makolo ao chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi, anthu odziwitsitsa ntchito ya utumiki wa nyumba ya Mulungu.
Mwa omveka anu muli ana aakazi a mafumu; ku dzanja lanu lamanja aima mkazi wa mfumu wovala golide wa ku Ofiri.
Ndipo ndidzachepsa anthu koposa golide, ngakhale anthu koposa golide weniweni wa ku Ofiri.
Ndipo Saulo anakantha Aamaleke, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri, chili pandunji pa Ejipito.