Genesis 10:25 - Buku Lopatulika Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana aamuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kwa Eberi ndipo kunabadwa ana amuna awiri; dzina la wina ndi Pelegi; chifukwa kuti m'masiku ake dziko lapansi linagawanikana; dzina la mphwake ndi Yokotani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Eberi anali ndi ana aŵiri. Wina anali Pelegi, chifukwa pa nthaŵi ya moyo wake, anthu onse a pa dziko lapansi anali ogaŵikana. Dzina la mbale wake linali Yokotani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero A Eberi anabereka ana aamuna awiri: Wina anamutcha Pelegi chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani. |
Amenewo ndi mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yao, m'mitundu yao: ndi amenewo anagawanika mitundu padziko lapansi, chitapita chigumula.
Amenewo ndipo anagawa zisumbu za amitundu m'maiko mwao, onse amene monga mwa chinenedwe chao; ndi mwa mabanja ao, ndi m'mitundu yao.
Ndi Eberi anabala ana aamuna awiri, dzina la winayo ndiye Pelegi, popeza masiku ake dziko linagawanika; ndi dzina la mbale wake ndiye Yokotani.
ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;
Pamene Wam'mwambamwamba anagawira amitundu cholowa chao, pamene anagawa ana a anthu, anaika malire a mitundu ya anthu, monga mwa kuwerenga kwao kwa ana a Israele.