Genesis 10:22 - Buku Lopatulika Ana aamuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana amuna a Semu; Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Semu anali Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu. |
Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakisadi, chitapita chigumula zaka ziwiri;
Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente a siliva chikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lake.
Akali chilankhulire uyu, anadza winanso, nati, Ababiloni anadzigawa magulu atatu, nazigwera ngamira, nazitenga, nawapha anyamata ndi lupanga lakuthwa, ndipo ndapulumuka ine ndekha kudzakuuzani.
Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti Ambuye adzabweza kachiwiri ndi dzanja lake anthu ake otsala ochokera ku Asiriya, ndi ku Ejipito, ndi ku Patirosi, ndi ku Kusi, ndi ku Elamu, ndi ku Sinara, ndi ku Hamati, ndi ku zisumbu za m'nyanja.
Masomphenya ovuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Mediya iwe; kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza.
Ndipo Elamu anatenga phodo, ndi magaleta a anthu ndi apakavalo; ndipo Kiri anaonetsa zikopa.
Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.
Elamu ali komwe ndi gulu lake lonse lozinga manda ake; ophedwa onsewo, adagwa ndi lupanga; amene anatsikira osadulidwa kunsi kwake kwa dziko, amene anaopsetsa m'dziko la amoyo, nasenza manyazi ao, pamodzi ndi iwo akutsikira kudzenje.
Ndipo ndinaona m'masomphenya; tsono kunali, pakuwaona ine ndinali mu Susa, m'nyumba ya mfumu, ndiwo m'dziko la Elamu; ndinaona m'masomphenya kuti ndinali kumtsinje Ulai.
Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ku Aramu ananditenga Balaki, mfumu ya Mowabu ananditenga ku mapiri a kum'mawa, Idza, udzanditembererere Yakobo. Idza, nudzanyoze Israele.
Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala mu Mesopotamiya, mu Yudeya, ndiponso mu Kapadokiya, mu Ponto, ndi mu Asiya;