Amenewa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
Genesis 10:21 - Buku Lopatulika Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Eberi, mkulu wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso kwa Semu atate wa ana onse a Eberi, mkulu wa Yafeti, kwa iye kunabadwa ana. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Semu ndiye kholo la ana onse a Eberi, ndiponso ndiye mkulu wake wa Yafeti. Iyeyu anali ndi ana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi. |
Amenewa ndi ana aamuna a Hamu monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.
Ana a Semu: Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu, ndi Uzi, ndi Huli, ndi Getere, ndi Meseki.
Koma zombo zidzafika kuchokera ku dooko la Kitimu, ndipo adzasautsa Asiriya, nadzasautsa Eberi, koma iyenso adzaonongeka.