Ndi Aisraele a ana a Parosi: Ramiya, ndi Iziya, ndi Matikiya, ndi Miyamini, ndi Eleazara, ndi Malikiya, ndi Benaya.
Ezara 2:3 - Buku Lopatulika ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ana a Parosi, zikwi ziwiri ndi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa A banja la Parosi, 2,172. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zidzukulu za Parosi 2,172 |
Ndi Aisraele a ana a Parosi: Ramiya, ndi Iziya, ndi Matikiya, ndi Miyamini, ndi Eleazara, ndi Malikiya, ndi Benaya.
ndiwo amene adadza ndi Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu, Baana. Kuwerenga kwa amuna a anthu a Israele ndiko:
Ndipo akulu a nyumba za makolo ndi awa, ndi chibadwidwe cha iwo okwera nane limodzi kuchokera ku Babiloni, pokhala mfumu Arita-kisereksesi, ndi ichi:
Wa ana a Sekaniya, wa ana a Parosi, Zekariya; ndi pamodzi naye, powawerenga monga mwa chibadwidwe chao, amuna zana limodzi mphambu makumi asanu.
Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene ili kubwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.