Eksodo 40:24 - Buku Lopatulika Ndipo anaika choikaponyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaika choikapo nyali m'chihema chokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwera ya Kachisi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'chihema chamsonkanomo adaikamo choikaponyale mopenyana ndi tebulo chakumwera kwake kwa malo opatulika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anayikanso choyikapo nyale mu tenti ya msonkhano moyangʼanana ndi tebulo mbali yakummwera kwa chihema. |
Nuziika gomelo kunja kwa nsalu yotchinga, ndi choikaponyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwera ya chihema; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto.
Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zake; ulongenso choikaponyalicho, ndi kuyatsa nyali zake.
Pamenepo Yesu analankhulanso nao, nanena, Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.
chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.
Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.