guwa la nsembe la mkuwa, ndi sefa wake wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake;
Eksodo 39:40 - Buku Lopatulika nsalu zotchingira za pabwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, zingwe zake, ndi zichiri zake, ndi zipangizo zonse za ntchito ya Kachisi, za ku chihema chokomanako; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nsalu zochingira za pabwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, zingwe zake, ndi zichiri zake, ndi zipangizo zonse za ntchito ya Kachisi, za ku chihema chokomanako; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adabweranso ndi nsalu zochingira bwalo pamodzi ndi nsanamira zake ndi masinde ake, nsalu yochingira pa chipata choloŵera m'bwalolo, pamodzi ndi zingwe zake ndi zikhomo zake, ndiponso zipangizo zonse zotumikira nazo m'chihema cha Chauta chija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; zingwe zake ndi zikhomo za tenti; zipangizo zonse za chihema, tenti ya msonkhano; |
guwa la nsembe la mkuwa, ndi sefa wake wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake;
zovala zokoma za kutumikira nazo m'malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe.
Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.