Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;
Eksodo 39:37 - Buku Lopatulika choikaponyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 choikapo nyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa choikaponyale cha golide wabwino kwambiri, nyale zake pamodzi ndi zipangizo zake, mafuta anyale; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri pamodzi ndi nyale zake ndi zipangizo zake zonse, ndiponso mafuta anyalezo; |
Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;
Ndipo uuze ana a Israele akutengere mafuta a azitona oyera opera akuunikira, kuti awalitse nyali kosalekeza.
Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.
ndi guwa la nsembe lagolide, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho;
Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikaponyalicho.
Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikaponyali, monga Yehova adauza Mose.
kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,