Ndipo Solomoni anapanga zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova: guwa la nsembe lagolide, ndi gome lagolide loikapo mikate yoonekera;
Eksodo 39:36 - Buku Lopatulika gomelo, zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 gomelo, zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adabweranso ndi tebulo, pamodzi ndi zipangizo zake, ndipo adaika buledi woperekedwa kosalekeza kwa Mulungu; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero tebulo pamodzi ndi zipangizo zake ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova; |
Ndipo Solomoni anapanga zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova: guwa la nsembe lagolide, ndi gome lagolide loikapo mikate yoonekera;
choikaponyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira;
Ndipo uzitenga ufa wosalala, ndi kuphika timitanda khumi ndi tiwiri; awiri a magawo khumi a efa afikane kamtanda kamodzi.
Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.