Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.
Eksodo 39:35 - Buku Lopatulika likasa la mboni, ndi mphiko zake, ndi chotetezerapo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 likasa la mboni, ndi mphiko zake, ndi chotetezerapo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa bokosi loikamo miyala yaumboni pamodzi ndi nsanamira zake, ndiponso chivundikiro cha bokosilo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero bokosi la umboni pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake; |
Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.
ndi chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiirira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi nsalu yotchinga yotsekera;
ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitingathe kunena tsopano paderapadera.
Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo kumalo opatulika siinaonetsedwe, pokhala chihema choyamba chili chilili;