Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti chihema chikhale chimodzi.
Eksodo 39:33 - Buku Lopatulika Ndipo anabwera naye Kachisi kwa Mose, chihemacho, ndi zipangizo zake zonse, zokowera zake, matabwa ake, mitanda yake, ndi mizati yake, nsanamira zake ndi nsichi zake, ndi makamwa ake; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anabwera naye Kachisi kwa Mose, chihemacho, ndi zipangizo zake zonse, zokowera zake, matabwa ake, mitanda yake, ndi mizati yake, nsanamira zake ndi nsichi zake, ndi makamwa ake; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake zonsezo adabwera nazo kwa Mose: chihema chija chodzakhala Nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ngoŵe zake zokoŵera, mafulemu ake, mitanda yake, nsanamira zake ndi masinde ake omwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka anabweretsa chihema kwa Mose. Tenti ndi zipangizo zake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake; |
Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolide, ndi kumanga nsaluzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti chihema chikhale chimodzi.
Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.
ndi chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiirira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi nsalu yotchinga yotsekera;