Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 39:28 - Buku Lopatulika

ndi nduwira yabafuta wa thonje losansitsa, ndi akapa okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zovala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa,

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi nduwira yabafuta wa thonje losansitsa, ndi akapa okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zovala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa,

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

nduŵira, makofiya ndi akabudula, zonsezo zopangidwa ndi nsalu ya bafuta wosalala ndi wopikidwa bwino.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

nduwira ya nsalu yofewa yosalala, lamba wa nsalu yofewa yosalala, womanga mʼmutu, ndi makabudula amʼkati a nsalu yofewa yosalala olukidwa bwino.

Onani mutuwo



Eksodo 39:28
11 Mawu Ofanana  

Ndipo polowa mutu pakhale pakati pake; pakhale mkawo pozungulira polowa pake, wa ntchito yoomba, ngati polowa pa malaya otchinjiriza, pangang'ambike.


Ndipo upikule malaya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika.


Ndipo zovala azisoka ndi izi: chapachifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ake zovala zopatulika, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Ndipo usokere ana a Aroni malaya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma.


Uwasokerenso zovala za miyendo za bafuta wa thonje losansitsa kubisa maliseche ao; ziyambire m'chuuno zifikire kuntchafu.


Ndipo anaomba malaya a bafuta, a ntchito yoomba, a Aroni, ndi a ana ake aamuna,


ndi mpango wabafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ntchito ya wopikula; monga Yehova adamuuza Mose.


ndi zisada, ndi maunyolo a kumwendo, ndi mipango, ndi nsupa zonunkhira, ndi mphinjiri;


Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.


Akhale nao akapa abafuta pamitu pao, ndi akabudula m'chuuno mwao; asavale m'chuuno kanthu kalikonse kakuchititsa thukuta.


Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto paguwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.