Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;
Eksodo 39:26 - Buku Lopatulika Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono panali khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, khangaza limodzi ndi kabelu kamodzi, kuzungulira mpendero wonse wa mkanjo, umene ansembe ankavala pogwira ntchito zaunsembe, monga momwe Chauta adalamulira Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero panali mphonje imodzi ndi belu limodzi kuzungulira mpendero wa mkanjo wovala potumikira monga momwe Yehova analamulira Mose. |
Ndipo pa mbinyiru wake upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, pambinyiru pake pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolide pozungulira;
mliu wa golide ndi khangaza, mliu wagolide ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira.
Ndipo anapanga miliu ya golide woona, napakiza miliu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza.
Milomo yako ikunga mbota yofiira, m'kamwa mwako ndi kukoma: Palitsipa pako pakunga phande la khangaza paseri pa chophimba chako.
Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake;