Eksodo 39:19 - Buku Lopatulika Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pansonga ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake m'katimo, pa mbali ya kuefodi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pa nsonga ziwiri za chapachifuwa, m'mphepete mwake m'katimo, pa mbali ya kuefodi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adapanga mphete ziŵiri zagolide, nazilumikiza ku nsonga ziŵiri za chovala chapachifuwa cham'mphepete, m'kati mwake, pafupi ndi chovala cha efodi chija. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anapanganso mphete ziwiri zagolide ndipo analumikiza ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija. |
Ndi nsonga zake ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwake.
Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pake, pa mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi.