ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.
Eksodo 39:17 - Buku Lopatulika Ndipo anamanga maunyolo awiri opota agolide pa mphete ziwiri pansonga za chapachifuwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anamanga maunyolo awiri opota agolide pa mphete ziwiri pa nsonga za chapachifuwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono zingwe ziŵiri zagolide adazilumikiza ku mphete ziŵiri zija, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anamangirira timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho. |
ndi maunyolo awiri a golide woona; uwapote ngati zingwe, ntchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo.
Anapanganso zoikamo ziwiri zagolide, ndi mphete ziwiri zagolide; naika mphete ziwirizo pansonga ziwiri za chapachifuwa.
Ndi nsonga zake ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m'tsogolo mwake.