Ndipo uzipangira nsalu yotsekerayo nsanamira zisanu za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide; nuziyengera makamwa asanu amkuwa.
Eksodo 38:30 - Buku Lopatulika Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi sefa wake amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi sefa wake amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ndi mkuŵa umenewu adapanga masinde a pa chipata choloŵera ku chihema chamsonkhano. Adapanganso guwa la nsembe zopsereza, pamodzi ndi chitsulo cha sefa, zipangizo zonse za guwalo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anawugwiritsa ntchito popanga matsinde a pa chipata cha tenti ya msonkhano, guwa la mkuwa pamodzi ndi sefa yake ndiponso ziwiya zonse, |
Ndipo uzipangira nsalu yotsekerayo nsanamira zisanu za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide; zokowera zao zikhale zagolide; nuziyengera makamwa asanu amkuwa.
ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Nsichi zonse za pabwalo pozungulira zimangike pamodzi ndi mitanda yasiliva; zokowera zao zasiliva, ndi makamwa ao amkuwa.
Ndipo uzipanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zikhale zotuluka m'mwemo: nulikute ndi mkuwa.
Ndipo ulipangire sefa, malukidwe ake ndi amkuwa; nupange pa malukidwewo ngodya zake zinai mphete zinai zamkuwa.
Ndi mkuwa wa choperekacho ndiwo matalente makumi asanu ndi awiri, ndi masekeli zikwi ziwiri kudza mazana anai.
ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku chipata cha pabwalo, ndi zichiri zonse za chihema, ndi zichiri zonse za pabwalo pozungulira.