Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kuiika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wake wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzake mikono isanu.
Eksodo 38:17 - Buku Lopatulika Ndipo makamwa a nsichi anali amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva; ndi zokutira mitu yake zasiliva; ndi nsichi zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo makamwa a nsichi anali amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva; ndi zokutira mitu yake zasiliva; ndi nsichi zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Masinde a nsanamirazo anali opangidwa ndi mkuŵa. Ndipo ngoŵe za pa nsanamirazo, mitanda yake ndi zokutira nsonga za nsanamirazo, zonsezo zinali zasiliva. Nsanamira zonse za bwalolo zidalumikizidwa ndi mitanda yasiliva. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Matsinde amizati anali amkuwa. Ngowe ndi zingwe za mizati zinali zasiliva, ndipo pamwamba pa mizatiyo anakutapo siliva. Choncho mizati yonse ya bwalolo inalumikizidwa ndi zingwe zasiliva. |
Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kuiika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wake wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzake mikono isanu.
ndi nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri akhale amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zikhale zasiliva.
Ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo ndiyo ntchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake ndi kupingasa kwake mikono isanu, yolingana ndi nsalu zotchingira za pabwalo.
Ndipo choyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a chihema, ndi mitanda yake, ndi mizati ndi nsanamira zake, ndi makamwa ake, ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito zake zonse;
ndi nsichi za kubwalo kozungulira, ndi makamwa ake, ndi zichiri zake, ndi zingwe zake, pamodzi ndi zipangizo zake zonse, ndi ntchito yake yonse; ndipo muziwerenga zipangizo za udikiro wa akatundu ao ndi kuwatchula maina ao.