Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake.
Eksodo 37:26 - Buku Lopatulika Ndipo analikuta ndi golide woona, pamwamba pake, ndi mbali zake pozungulira, ndi nyanga zake; ndipo analipangira mkombero wagolide pozungulira pake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo analikuta ndi golide woona, pamwamba pake, ndi mbali zake pozungulira, ndi nyanga zake; ndipo analipangira mkombero wagolide pozungulira pake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakuta guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri pamwamba pake, pa mbali zake ndi pa nyanga zake zomwe. Kuzungulira guwa lonselo, adalemba mkombero wagolide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anakuta guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse ndi nyanga zake, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira guwalo. |
Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake.
Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wakasiya; utali wake mkono, ndi kupingasa kwake mkono, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zinatuluka m'mwemo.
Ndipo analipangira mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake, pangodya zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri, zikhale zopisamo mphiko kulinyamulira nazo.