Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziwiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golide woona.
Eksodo 37:24 - Buku Lopatulika Anachipanga ichi ndi zipangizo zake zonse za talente wa golide woona. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anachipanga ichi ndi zipangizo zake zonse za talente wa golide woona. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Popanga choikaponyalecho, pamodzi ndi zipangizo zake zonsezo, adagwiritsa ntchito makilogaramu 34 a golide wabwino kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anapanga choyikapo nyale ndi zipangizo zake zonse zagolide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34. |
Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziwiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golide woona.
Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wakasiya; utali wake mkono, ndi kupingasa kwake mkono, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zinatuluka m'mwemo.