Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 37:22 - Buku Lopatulika

Mitu yao ndi mphanda zao zinatuluka m'mwemo; chonsechi chinali chosulika pamodzi cha golide woona.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mitu yao ndi mphanda zao zinatuluka m'mwemo; chonsechi chinali chosulika pamodzi cha golide woona.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nkhunjezo, pamodzi ndi nthambizo, zidapangidwira kumodzi ndi choikaponyale chija. Chonsecho chinali chinthu chimodzi chagolide, chosula ndi nyundo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mphukira ndi nthambi zonse zinasulidwa kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri.

Onani mutuwo



Eksodo 37:22
9 Mawu Ofanana  

Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.


Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;


Mitu yao ndi mphanda zao zikhale zotuluka m'mwemo; chonsechi chikhale chosulika chimodzi cha golide woona.


ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zochokera m'mwemo.


Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziwiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golide woona.


Chifukwa kuti munda wampesa wa madera khumi udzangobala bati imodzi ya vinyo, ndi mbeu za maefa khumi zidzangobala efa imodzi.


koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.


Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;